Eksodo 27:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Upange nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo kuti nyangazo ndi guwalo zikhale chinthu chimodzi, ndipo ulikute guwalo ndi mkuwa. Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Upange nyanga pa ngodya zake zinaizo, zilumikizane ndi guwalo, ndipo ulikute ndi mkuŵa. Onani mutuwo |
Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo.