Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 26:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa Kachisi; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Uwombenso nsalu khumi ndi imodzi za ubweya wambuzi kuti zikhale lona lophimba pamwamba pa chihemacho.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:7
18 Mawu Ofanana  

Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.


Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi;


“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.


Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho.


Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.


Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi.


Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri.


Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri.


Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa.


Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi.


nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi;


Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova.


Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano,


Muyeretsenso zovala zanu ndi china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ubweya wa mbuzi kapenanso ndi mtengo.”


Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano,


Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.


Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa