Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 26:19 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

19 Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndipo upange masinde makumi anai asiliva pansi pa mafulemu makumi aŵiriwo. Pansi pa fulemu lililonse pakhale masinde aŵiri ogwirizira zolumikizira ziŵiri zija.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:19
14 Mawu Ofanana  

Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere.


Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho.


Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri.


Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse.


Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”


Upangenso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa, ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.


Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi.


Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi.


Miyendo yake ili ngati mizati yamwala, yokhazikika pa maziko a golide. Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni, abwino kwambiri ngati mkungudza.


Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa