Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 24:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe pa phiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ulemerero wa Chauta udatsikira pa phiri la Sinai, ndipo lidaphimbidwa ndi mtambo masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri Chauta adaitana Mose m'kati mwa mtambomo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 24:16
14 Mawu Ofanana  

Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo; iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.


Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.


ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona.


Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena.


Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu.


Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo.


Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova.


Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.


Ndipo Mose pamodzi ndi Aaroni analowa mu tenti ya msonkhano. Atatulukamo anadalitsa anthuwo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.


Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”


Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano.


Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera.


Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.


Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa