Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 23:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Musazunze mlendo. Inu nomwe mukudziŵa m'mene amamvera mlendo, poti paja inunso munali alendo ku Ejipito kuja.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 23:9
13 Mawu Ofanana  

Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye.


Koma ngati kapolo uja akhala ndi moyo tsiku lonse kapena masiku awiri, ndiye kuti mbuye uja asalangidwe chifukwa kapolo ndi chuma chake.


“Aliyense wopereka nsembe kwa mulungu wina osati Yehova awonongedwe.


“Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto.


Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo.


Mu mzindamo anthu amanyoza abambo ndi amayi awo. Iwo amapondereza alendo ndi kuzunza ana amasiye ndi akazi amasiye.


“ ‘Pamene mlendo akhala nanu mʼdziko mwanu, musamuzunze.


Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’


Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto.


Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake.


“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa