Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 23:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 23:1
40 Mawu Ofanana  

Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane.


Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?” Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”


Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani.


Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.


Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?


ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,


Musandipereke ku zokhumba za adani anga, pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane ndipo zikundiopseza.


Mboni zopanda chisoni zinayimirira, zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.


“Usapereke umboni womunamizira mnzako.


Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.


Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.


Woyankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yabodza imafotokoza zonama.


Mboni yokhulupirika sinama, koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.


Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa; munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.


Mboni yopanda pake imanyoza cholungama, ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.


Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.


Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.


Mboni yonama idzawonongeka, koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.


Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.


Munthu wochitira mnzake umboni wonama, ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.


Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula, chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.


mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.


Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti, “Zoopsa ku mbali zonse! Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!” Onse amene anali abwenzi anga akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti, “Mwina mwake adzanyengedwa; tidzamugwira ndi kulipsira pa iye.”


“ ‘Musabe. “ ‘Musamanamizane. “ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.


“ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu. “ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.


Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?” Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama,


Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”


Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”


“Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”


Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera.


Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi.


“Usapereke umboni womunamizira mnzako.


Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino,


Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho.


Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti, “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera. Pakuti woneneza abale athu uja, amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku, wagwetsedwa pansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa