Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 21:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mukagula kapolo wachihebri, adzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Muzidzammasula pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, iye osalipirapo kanthu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:2
18 Mawu Ofanana  

Mulungu akugwetsere mame akumwamba ndipo minda yako ibale tirigu wambiri ndi vinyo watsopano.


Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”


Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, “Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake.”


ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene.


Kapolo aliyense amene munagula angadye ngati atayamba wachita mdulidwe.


Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso.


“Ngati munthu agulitsa mwana wake wamkazi kukhala mdzakazi, mwanayo asamasulidwe monga achitira ndi akapolo aamuna.


Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo.


“ ‘Ngakhale munthuyo atapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, iye ndi ana ake ayenera kumasulidwa mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu,


Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo.


Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.


Kumapeto kwa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, muzikhululukirana ngongole.


Musaone ngati chopweteka kumasula wantchito wanu, chifukwa ntchito imene wayigwira pa zaka zisanu ndi chimodzi zimenezi ndi yopindula kawiri pa ntchito imene akanagwira waganyu chabe. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita.


Kenaka Mose anawalamula kuti, “Pamapeto pa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, chaka cha kukhululukidwa ngongole, pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa