Eksodo 21:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 “Uwawuze Aisraeli malamulo awa: Onani mutuwoBuku Lopatulika1 Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 “Tsono Aisraele uŵalangize izi: Onani mutuwo |
Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.
tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi.