Eksodo 20:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 “Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha. Onani mutuwo |
Kawirikawiri ndakhala ndikutumiza atumiki anga, aneneri, kwa inu. Iwo akhala akukuwuzani kuti, ‘Aliyense wa inu asiye ntchito zake zoyipa ndi kukonza makhalidwe ake; musatsatire milungu ina ndi kumayitumikira. Pamenepo mudzakhala mʼdziko limene ndinakupatsani ndi makolo anu.’ Komabe inu simunasamale zimenezi kapena kundimvera Ine.
Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu.