Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 2:17 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Koma kunabwera abusa ena amene anathamangitsa atsikana aja. Ndiye Mose anayimirira nawathandiza atsikana aja ndi kumwetsa nkhosa zawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

17 Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma kudabwera abusa ena naŵapirikitsa atsikanawo. Apo Mose uja adaimirira naŵathandiza atsikana aja, ndipo adamwetsa zoŵeta zao zonse zija.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:17
5 Mawu Ofanana  

Kenaka Abrahamu anadandaula kwa Abimeleki pa za chitsime chimene antchito a Abimeleki analanda.


Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa amayi ake, ali ndi nkhosa za Labani, anapita nawugudubuza mwala uja nazimwetsa madzi nkhosa za amalume akezo.


Amati nkhosa zonse zikasonkhana, abusawo ankagudubuza mwalawo, kuwuchotsa ndi kumwetsa madzi nkhosazo. Kenaka ankawubwezera mwalawo pamalo pake, pakamwa pa chitsimepo.


Atayangʼana uku ndi uku, naona kuti panalibe wina aliyense, Mose anamupha Mwiguptoyo ndipo anamukwirira mu mchenga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa