Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 2:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana aakazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Amene anali wansembe ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi aŵiri. Ana aakaziwo adabwera kudzatunga madzi, kuti adzaze m'chomwera nkhosa ndi mbuzi za bambo wao.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:16
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba,


Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.


Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi.


Atafika kumeneko anaona chitsime ku busa ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pafupi ndi chitsimecho chifukwa nkhosazo zimamwetsedwa madzi ochokera mʼchitsimecho. Pamwamba pa chitsimecho panali mwala waukulu.


Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto.


Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.


Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.


Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu.


Akukwera phiri kupita ku mzindawo anakumana ndi atsikana akutuluka mu mzindamo kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa