Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 19:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera. Tsono ukaŵauze mau ameneŵa Aisraele.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:6
37 Mawu Ofanana  

Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga.


Pakuti Inu munawasiyanitsa ndi anthu a mitundu ina yonse ya dziko lonse kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munanenera kudzera mwa mtumiki wanu Mose pamene Inu, Ambuye Yehova, munatulutsa makolo athu ku Igupto.”


Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.


Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake.


Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”


“Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.”


“Upange duwa lagolide wabwino kwambiri kukhala ngati chidindo ndipo uzokotepo mawu akuti, choperekedwa kwa Yehova.


Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga, ndipo chifukwa ndimakukonda, ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.


Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova, adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu. Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.


Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika, owomboledwa a Yehova; ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova” “Mzinda umene Yehova sanawusiye.”


Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.


Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.


Israeli anali wopatulika wa Yehova, anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola; onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa ndipo mavuto anawagwera,’ ” akutero Yehova.


koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.


“Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.


Koma Ine ndinakuwuzani kuti, ‘Mudzatenga dziko lawo. Ine ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale cholowa chanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.


Muzikhala woyera pamaso panga chifukwa Ine Yehova, ndine woyera ndipo ndakupatulani pakati pa anthu a mitundu yonse kuti mukhale anthu anga.


Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’ ”


“Inu nokha ndi amene ndinakusankhani pakati pa mabanja onse a dziko lapansi; nʼchifukwa chake ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu onse.”


‘Izi ndi zimene ndinapangana nanu pamene munkatuluka ku Igupto. Ndipo Mzimu wanga uli pakati panu. Musachite mantha.’


Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?”


Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.


Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.


Musamadye chilichonse chimene mwachipeza chofaifa. Mukhoza kupatsa mlendo amene akukhala mu mzinda wina uliwonse wa mizinda yanu. Iyeyo akhoza kudya kapena mukhoza kugulitsa kwa wina aliyense amene sali wa mtundu wanu. Koma inu ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Musamaphike mwana wambuzi mu mkaka wa mayi wake.


Iye wanenetsa kuti adzakuyikani kukhala oyamikika, otchuka ndi olemekezeka koposa mitundu yonse imene anayilenga. Komanso mudzakhala anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu monga momwe analonjezera.


Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti mukhale anthu ake opatulika, monga momwe analonjezera pa malumbiro ake, ngati musunga malamulo ake ndi kuyenda mʼnjira zake.


Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali.


Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.


inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.


ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.


Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.


Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu, ndipo adzalamulira dziko lapansi.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa