Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 19:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere cha Aisraele ku Ejipito, mpamene adafika ku chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:1
16 Mawu Ofanana  

“Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka.


Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”


Muzisunge mpaka tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi, pamene gulu lonse la Aisraeli lidzaphe nyamazo madzulo.


Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai.


Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.”


“Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.


Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kubwera nawo mʼchipululu.


Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,


Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani.


Yehova anawuza Mose mʼchipululu cha Sinai kuti,


Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai


Ku Horebu, Yehova Mulungu wathu anati kwa ife, “Mwakhalitsa pa phiri lino.


Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.”


Tsiku limene Yehova anayankhula nanu ku Horebu mʼmoto uja, simunaone thupi lake. Choncho mudziyangʼanire nokha mosamalitsa,


Yehova Mulungu wathu anachita pangano ndi ife ku Horebu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa