Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 18:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Mose adamchingamira nakakumana naye, ndipo adamgwadira ndi kumumpsompsona. Atalonjerana ndi kufunsana za moyo, adakaloŵa mu hema.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:7
23 Mawu Ofanana  

Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).


Tsono Abrahamu atakweza maso ake patali anangoona anthu atatu atayima cha potero. Atawaona, ananyamuka mofulumira kuti awachingamire. Atafika anaweramitsa mutu pansi mwa ulemu nati,


Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu.


Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika.


Sunandilole kuti ndingopsompsona adzukulu anga ndi ana anga aakazi motsanzikana nawo. Unachita zopusa.


Yosefe atafika ku nyumbako, iwo anapereka mphatso zija namuweramira pansi.


Atatero, Yosefe anapsompsona abale ake onse aja, akulira. Pambuyo pake abale ake aja anacheza ndi Yosefe.


Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.


Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera.


Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.


Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.


Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”


Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa.


Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona.


Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake.


Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga.


Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona.


Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa.


Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.


Utengerenso wolamulira wa gulu lawo tchizi khumi uyu. Ukaone mmene abale ako akukhalira ndipo ubwere ndi kanthu kosonyeza kuti ali bwino.


Tsono Davide anasiyira zakudya zija munthu wosunga katundu nathamangira kumene kunali ankhondo kuja ndi kukalonjera abale ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa