Eksodo 18:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.” Onani mutuwoBuku Lopatulika16 akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Anthu aŵiri akamakangana, amabwera kwa ine, ndipo ndimaŵaweruza, ndi kuwona kuti wakhoza ndani. Ndipo ndimaŵauza mau a Mulungu ndi malamulo ake.” Onani mutuwo |
Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.