Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 18:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamenepo Yetero adapereka kwa Mulungu nsembe yopsereza ndi nsembe zinanso. Kenaka Aroni ndi atsogoleri a Aisraele adabwera pamaso pa Mulungu kudzadya pamodzi ndi Yetero mpongozi wa Mose.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:12
31 Mawu Ofanana  

Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.


Isake anamanga guwa lansembe pamenepo ndipo anapembedza Yehova. Pomwepo anamanga tenti yake, ndipo antchito ake anakumba chitsime.


Tsono Isake anawakonzera phwando, ndipo anadya ndi kumwa.


Yakobo anapereka nsembe pa phiri paja, ndipo anayitana abale ake kuti adzadye chakudya. Atadya chakudya anagona pa phiri pomwepo.


Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake.


Abale aja anakonzeratu mphatso zawo zija kuti adzapereke kwa Yosefe, popeza anamva kuti Yosefe adzadya komweko masana.


Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza.


Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”


Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.


Masiku aphwandowo atatha, Yobu ankawayitana kuti adzawayeretse. Mmamawa iye ankapereka nsembe yopsereza kuperekera mwana aliyense, poganiza kuti, “Mwina ana anga achimwa ndi kutukwana Mulungu mʼmitima yawo.” Umu ndi mmene Yobu ankachitira nthawi zonse.


Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.


Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.”


Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo.


Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo.


Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.”


Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani.


Ngakhale anaona Yehova koma sanafe, mʼmalo mwake anadya ndi kumwa.


Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano.


Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu.


Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa.


Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.


Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”


Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa.


Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”


Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo?


Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda.


Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


Kumeneko, pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalalako pa china chilichonse chimene mudzakhudza, chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.


Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa