Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 18:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo Yetero, wansembe wa Midiyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israele anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israele mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yetero, wansembe wa Midiyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israele anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israele m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yetero, wansembe wa ku Midiyani, mpongozi wake wa Mose, adamva zonse zija zimene Mulungu adachitira Mose ndiponso anthu ake Aisraele. Adamvanso za m'mene Chauta adaŵatulutsira ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:1
33 Mawu Ofanana  

Iye anatulutsa anthu ake akukondwera, osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;


Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita, zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,


Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova kapena kumutamanda mokwanira?


Moyo wanga udzanyadira Yehova; anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.


Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.


Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.


Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo.


Atsikana aja atabwerera kwa abambo awo Reueli, iye anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero mwabwera msanga?”


Mose anavomera kukhala ndi Reueli, ndipo anamupatsa Zipora kuti akhale mkazi wake.


Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu.


Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.” Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.”


“Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo.


Mzinda wa Yerusalemu udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemerero. Anthu a mitundu yonse adzanditamanda akadzamva za zabwino zonse zimene ndawuchitira mzindawu. Iwo adzachita mantha ndi kunjenjemera poona madalitso ochuluka ndi mtendere zimene ndapereka kwa mzinda umenewu.’


Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a ziyankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nawo, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ”


Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”


Atangofika ku Antiokeya, anasonkhanitsa pamodzi mpingo ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo ndiponso mmene Iye anatsekulira a mitundu ina njira ya chikhulupiriro.


Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo.


Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita


Ife tinamva mmene Yehova anawumitsira madzi a Nyanja Yofiira inu mukufika pamene munatuluka mʼdziko la Igupto. Tamvanso zimene munachita kwa Sihoni ndi Ogi, mafumu awiri a Aamori amene ali kummawa kwa Yorodani. Inu munawawononga kotheratu.


Iwo anayankha kuti, “Akapolo anufe tachokera ku dziko lakutali chifukwa tamva za Yehova Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye anachita ku Igupto,


Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki.


Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa