Eksodo 17:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka. Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israele; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo mtsinje, numuke. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israele; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Tengako atsogoleri ena a Aisraele, mukakhale patsogolo pa anthuwo. Tsono utenge ndodo udamenya nayo madzi a mu mtsinje wa Nailo ija, ndipo upite. Onani mutuwo |