Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 16:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 m'maŵa mwake mudzaona ulemerero wa Chauta. Wamva madandaulo anu omuŵiringulira aja. Kodi ife ndife yani, kuti inu muzitiŵiringulira?”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:7
17 Mawu Ofanana  

Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.


“Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”


Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”


ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo.


Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo.


Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.


Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.


Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera, ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona, pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”


Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”


Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano.


“Kodi anthu oyipawa adzangʼungʼudza ndi kutsutsana nane mpaka liti? Ndamva madandawulo a Aisraeli ongʼungʼudzawa.


Nʼkulakwira Yehova kuti iwe ndi gulu lako lonseli mwasonkhana kuti mutsutsane ndi Yehova. Kodi Aaroni ndani kuti muzikangana naye?”


Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera.


Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.”


Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.”


Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa