Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 15:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova, dzanja lanu lamanja ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake. Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja linaphwanya mdani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero, chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:6
27 Mawu Ofanana  

Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu, Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.


Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”


Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.


Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.


Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.


Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja, kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.


Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!


Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso: zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.


Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu; chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso.


Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa?


Munatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko linawameza.


Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.


Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.


Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.


Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”


Lidzaphwanyika ngati mbiya imene yanyenyekeratu, mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhale lopalira moto mʼngʼanjo kapena lotungira madzi mʼchitsime.”


Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe, Inu Yehova; dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana, monga nthawi ya mibado yakale. Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe, amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?


Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika pamaso pa anthu a mitundu yonse, ndipo anthu onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,


Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”


Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’


Adzayilamulira ndi ndodo yachitsulo ndipo nadzayiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi omwe ndinalandira kwa Atate anga.


Yehova adzaphwanya omutsutsa. Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba; Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi. “Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake, adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa