Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 15:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati, “Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:1
27 Mawu Ofanana  

Inu munagawa nyanja anthu anu akupenya, kotero kuti anadutsa powuma, koma munamiza mʼmadzi akuya anthu amene ankawalondola monga mmene uchitira mwala mʼmadzi ozama.


Kumbukirani kutamanda ntchito zake zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.


Iye anatulutsa anthu ake akukondwera, osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;


Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake ndi kuyimba nyimbo zamatamando.


Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,


Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,


Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. Sela


Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo, kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.


Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.”


Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo.


Miriamu anawayimbira nyimbo iyi: “Imbirani Yehova, chifukwa iye wapambana. Kavalo ndi wokwerapo wake Iye wawamiza mʼnyanja.”


Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.”


Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake, koma wochita chilungamo amayimba lokoma.


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi, inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo. Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.


ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo, ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.


Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake; sadzatchulanso mayina awo popemphera.


komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.


Pamenepo Aisraeli anayimba nyimbo iyi: “Tulutsa madzi, chitsime iwe! Chiyimbireni nyimbo,


Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.


Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati, “Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona, Mfumu ya mitundu yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa