Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 13:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mudye buledi wopanda yisiti masiku asanu ndi awiri. Pasapezeke chinthu chilichonse chokhala ndi yisiti pakati panu, kapena paliponse mʼdziko lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisaoneke kwanu m'malire ako onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisaoneke kwanu m'malire ako onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pasamadzakhala buledi wofufumitsa, kapena chofufumitsira chilichonse m'dziko lanu lonselo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:7
6 Mawu Ofanana  

Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli.


Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa.


Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”


Choncho, tiyeni tisunge chikondwererochi, osati ndi yisiti wakale, wowononga ndi woyipa, koma ndi buledi wopanda yisiti, buledi woona mtima ndi choonadi.


Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.


Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa