Eksodo 12:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Adzawotche nyamayo ndi kudya usiku womwewo, ndipo adzayidye ndi buledi wophikidwa popanda yisiti pamodzi ndi masamba wowawa. Onani mutuwoBuku Lopatulika8 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Nyamayo adzaiwotche usiku womwewo, ndipo adzaidye ndi buledi wosafufumitsa ndiponso ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba. Onani mutuwo |
“Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa.