Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 12:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anayankhula kwa Mose ndi Aaroni mʼdziko la Igupto kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta adalankhula kwa Mose ndi Aroni m'dziko lija la Ejipito kuti,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:1
17 Mawu Ofanana  

Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.”


Aisraeli amene analipo anachita chikondwerero cha Paska pa nthawi imeneyi ndi kuchita mwambo wa chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti, kwa masiku asanu ndi awiri.


Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake.


Awuze anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnansi wake ziwiya zasiliva ndi golide.”


Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo.


“Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka.


Kenaka Yehova anati kwa Mose,


“Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi.


“ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi awiri. Pa masiku amenewo muzidzadya buledi wopanda yisiti.


“ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova.


“Aisraeli azichita Paska pa nthawi yake yoyikika.


Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.”


ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.


Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha.


Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira,


Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.


Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa