Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 11:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Yehova ananena kwa Mose kuti, “Farao adzakana kukumvera, kuti zodabwitsa zanga zichuluke mʼdziko la Igupto.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Chauta adauza Mose kuti, “Farao sadzakumvera iwe, kuti pakutero, Ine ndichite zozizwitsa m'dziko la Ejipito.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 11:9
5 Mawu Ofanana  

Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo


Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza.


Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa