Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 10:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 kuti inu mudzawuze ana ndi zidzukulu zanu za mmene ndinawakhawulitsira Aigupto ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinachita pakati pawo ndiponso kuti inu mudziwe kuti ine ndine Yehova.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita m'Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipo inu, mudzaŵauze ana anu ndi zidzukulu zanu za m'mene ndidapusitsira Aejipito, pamene ndinkachita zozizwitsa pakati pao. Motero nonsenu mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:2
22 Mawu Ofanana  

Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu.


Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.


Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena ndi kudzala makolo athu; Inu munakantha mitundu ya anthu, koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.


Ndipo anthu adzanena kuti, “Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho; zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”


Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu musanditaye Inu Mulungu, mpaka nditalengeza mphamvu zanu kwa mibado yonse yakutsogolo.


zimene tinazimva ndi kuzidziwa, zimene makolo athu anatiwuza.


“Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu.


Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.”


Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi.


Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova:


Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.”


Kotero Aaroni analoza dzanja lake pa madzi a ku Igupto, ndipo achule anatuluka nadzaza dziko lonse la Igupto.


Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani, monga mmene ndikuchitira ine lero lino; abambo amawuza ana awo za kukhulupirika kwanu.


Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’


Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa.


Muwafotokozere ana anu, ndipo ana anuwo afotokozere ana awo, ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.


Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.


Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa