Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 10:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mwamsangamsanga, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Ine ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndipo Farao adaitana Mose ndi Aroni mofulumira naŵauza kuti, “Ndachimwira Chauta, Mulungu wanu, ndipo ndachimwiranso inu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:16
14 Mawu Ofanana  

Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.”


Davide anatsutsika mu mtima mwake atatha kuwerenga anthuwo ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono Yehova, ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”


Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.”


Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu mʼdziko lomwe lino.”


Kenaka, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Pemphera kwa Yehova kuti achulewa achoke kwa ine ndi anthu anga, ndipo ine ndidzalola kuti anthu anu apite kukapereka nsembe kwa Yehova.”


Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa.


Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.


Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo.


Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.”


Iye anati, “Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa.” Iwo anayankha nati, “Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako.”


Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera.


Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.”


Ndipo Sauli anati, “Ine ndachimwa. Bwerera mwana wanga Davide. Sindidzakuchitanso choyipa popeza lero wauwona moyo wanga ngati wamtengowapatali. Taona, ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa