Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 10:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako padziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere padziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Ejipito kuti dzombe libwere, ndipo lidzadye zomera zonse zimene matalala aja adasiya.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:12
6 Mawu Ofanana  

Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera, ziwala zosawerengeka;


Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto.


Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.”


Koma tirigu ndi mchewere sizinawonongeke chifukwa zimakhwima mochedwa.


Ndipo mʼkati mwa utsimo munatuluka dzombe kukalowa mʼdziko lapansi ndipo linapatsidwa mphamvu zoluma ngati za zinkhanira pa dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa