Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli.