Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 1:15 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mfumu ya Igupto inati kwa azamba a Chihebri omwe mayina awo anali Sifira ndi Puwa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

15 Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono mfumu ya ku Ejipito ija idaitana azamba amene ankathandiza azimai achihebri pochira. Wina mwa azamba ameneŵa anali Sifira, wina anali Puwa. Mfumuyo idauza azambawo kuti,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:15
4 Mawu Ofanana  

Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi.


“Mukamathandiza amayi a Chihebri pa mwala wochirira, muzionetsetsa kuti akabadwa mwana wamwamuna muzipha, koma akakhala wamkazi muzimuleka akhale ndi moyo.”


Iye anayankha kuti, “Ndine Mhebri, ndipo ndimapembedza Yehova, Mulungu Wakumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.”


Koma nʼkuti atawakweza pa denga azondiwo ndi kuwabisa pansi pa mapesi a thonje amene iye anawayika pa dengapo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa