Danieli 9:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu. Onani mutuwoBuku Lopatulika5 tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu; Onani mutuwo |
Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata.