Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 9:23 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Utangoyamba kupemphera, Mulungu anayankha. Tsono ine ndabwera kudzakuwuza yankholo, popeza ndiwe wokondedwa kwambiri. Choncho mvetsetsa pamene ndikufotokoza za zinthu zimene unaziona mʼmasomphenya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

23 Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 9:23
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ”


Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.


Wokondedwayo ine ndine wake, ndipo chilakolako chake chili pa ine.


Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.


“Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.


Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja.


Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.


Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.” Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.”


Tsono Danieli anadzionetsa kuti akhoza kugwira ntchito bwino kopambana nduna zinzake chifukwa anali wanzeru kwambiri. Ndiye mfumu inaganiza zomuyika kuti akhale woyangʼanira ufumu wonse.


“Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire.


Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa