Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 9:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Monga kunalembedwa mʼMalamulo a Mose, tsoka lililonse latifikira chikhalirecho sitinapemphe Yehova Mulungu wathu kuti atikomere mtima. Sitinasiye machimo athu, ndipo sitinasamale choonadi chanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

13 Monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose choipa ichi chonse chatidzera; koma sitinapepese Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kuchita mwanzeru m'choonadi chanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose choipa ichi chonse chatidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kuchita mwanzeru m'choonadi chanu.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 9:13
35 Mawu Ofanana  

‘Ichi ndi chimene Yehova akunena: Taonani, ndidzabweretsa mavuto pa malo ano ndi pa anthu ake, molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga.


“Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo; akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.


Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.


Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu; pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.


Manja anu anandilenga ndi kundiwumba; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ndiphunzire malamulo anu.


Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.


Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo, amene amadalira akavalo, nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo, koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli, kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.


Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi, ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano; zinthuzo zisanaonekere Ine ndakudziwitsani.”


“Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo, munatopa nane, Inu Aisraeli.


Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa, ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo; tonse tafota ngati tsamba, ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.


Palibe amene amapemphera kwa Inu kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu; pakuti mwatifulatira ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.


Koma anthu sanabwerere kwa amene anawakantha uja, ngakhale kufunafuna Yehova Wamphamvuzonse.


“Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu; iwo sanaphunzirepo kanthu. Monga mkango wolusa, lupanga lanu lapha aneneri anu.


Abwenzi anu onse akuyiwalani; sasamalanso za inu. Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira. Ndipo ndakulangani mwa nkhanza, chifukwa machimo anu ndi ambiri, ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.


“Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti, ‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva. Koma inu mwatiphunzitsa kumvera. Mutibweze kuti tithe kubwerera, chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.


Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”


Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu.


Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona? Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka; munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala ndipo anakaniratu kulapa.


Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere; mukonzenso masiku athu akhale monga akale,


“ ‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.


Aisraeli onse anachimwira lamulo lanu motero anapatuka, nakana kukumverani. “Choncho matemberero ndi olumbira amene alembedwa mʼmalamulo a Mose, mtumiki wa Mulungu, atigwera chifukwa takuchimwirani.


Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa, koma pa zonsezi iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake kapena kumufunafuna.


Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima, koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo. Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano, koma amandifulatira.


Onsewa ndi otentha ngati uvuni, amapha olamulira awo. Mafumu awo onse amagwa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.


Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba.


Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,


Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine.


Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”


Zoonadi munamva za Iye ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye molingana ndi choonadi chimene chili mwa Yesu.


Koma mpaka lero Yehova sanakupatseni mtima wozindikira kapena maso openya kapena makutu akumva.


Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa