Danieli 7:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Zitatha izi, mʼmasomphenya anga usiku, ndinaonanso chirombo chachinayi chitayima patsogolo panga. Chinali choopsa, chochititsa mantha ndi champhamvu kwambiri. Chinali ndi mano akuluakulu a chitsulo. Chimati chikatekedza ndi kumeza adani ake kenaka chinapondereza chilichonse chotsala. Ichi chinali chosiyana ndi zirombo zoyambirira zija, ndipo chinali ndi nyanga khumi. Onani mutuwoBuku Lopatulika7 Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano akulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi. Onani mutuwo |
Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.