Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 7:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, napatsidwa ulamuliro.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, nichinapatsidwa ulamuliro.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 7:6
10 Mawu Ofanana  

Uwawuze kuti Ambuye Yehova akuti, chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko amphamvu, nthenga zitalizitali zamathothomathotho chinabwera ku Lebanoni. Chinagwira nthambi ya pamwamba pa mtengo wa mkungudza.


Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera.


“Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi.


“Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu.


“Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’


Motero ndidzawalumphira ngati mkango, ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.


Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa