Danieli 7:18 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’ Onani mutuwoBuku Lopatulika18 Koma opatulika a Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Koma opatulika a Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya. Onani mutuwo |
Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli ku dziko lawo. Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova. Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo. Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000.