Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 7:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 7:14
41 Mawu Ofanana  

pamene mitundu ya anthu ndi maufumu adzasonkhana kuti alambire Yehova.


Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.


Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.


Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse. Tamandani Yehova.


Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi; ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.


Mafumu onse adzamuweramira ndipo mitundu yonse idzamutumikira.


Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.


Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu; munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;


Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi; mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.


Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe; adzawonongeka kotheratu.


Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.


Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.


Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi.


Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero;


“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya.


“Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse


Zizindikiro zake ndi zazikulu, zozizwitsa zake ndi zamphamvu! Ufumu wake ndi wamuyaya; ulamuliro wake ndi wa mibadomibado.


“Ndikukhazikitsa lamulo kuti paliponse mʼdziko langa anthu ayenera kuopa ndi kuchitira ulemu Mulungu wa Danieli. “Popeza Iye ndi Mulungu wamoyo ndi wamuyaya; ufumu wake sudzawonongeka, ulamuliro wake sudzatha.


Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’


Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”


Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyoni ndipo adzalamulira mapiri a Esau. Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.


Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala. Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu. Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.


“Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.


Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.


ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”


“Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”


Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?”


Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake.


Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha.


amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.


ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.


Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”


Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”


Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa