Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 7:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

13 Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 7:13
39 Mawu Ofanana  

Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako.


Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.


Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.


“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani kupita ku malo a msipu wobiriwira, Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo. Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine. Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani? Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”


Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu.


“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya.


Zirombo zina zija zinalandidwa ulamuliro wawo, koma zinaloledwa kukhala ndi moyo kwa kanthawi.


Danieli anati, “Mʼmasomphenya anga usiku, ndinaona nyanga yayikulu ikuvunduka ndi mphepo zochokera mbali zonse zinayi za mlengalenga.


mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu.


“Ine ndikuyangʼanabe ndinaona “mipando yaufumu ikukhazikitsidwa, ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake. Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana; tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje. Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto, ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.


Ine Danieli ndikuyangʼanitsitsa masomphenyawa ndi kuyesa kuwazindikira, kuwamvetsa, ndinangoona wina wooneka ngati munthu atayima patsogolo panga.


Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa.


“Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.


“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba.


Yesu anayankha nati, “Mwanena ndinu. Koma ndikunena kwa inu nonse: mʼtsogolomo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba.”


Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.


Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ndi mbalame zamlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa Munthu alibe malo ogona ngakhale potsamira mutu wake.”


“Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero.


Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”


Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.


Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?”


Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu.


Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.


Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”


Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya.


Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.


Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa.


Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.


Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake.


Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.


“Onani akubwera ndi mitambo,” ndipo “Aliyense adzamuona, ndi amene anamubaya omwe.” Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.” Zidzakhaladi momwemo, Ameni.


Ndinayangʼana patsogolo panga ndinaona mtambo woyera patakhalapo wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chipewa chaufumu chagolide ndipo mʼdzanja mwake munali chikwakwa chakunthwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa