Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 6:18 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kenaka mfumu inabwerera ku nyumba yake ndipo inakhala usiku wonse osadya kanthu, osalola chosangalatsa chilichonse. Ndipo sinagone tulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

18 Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 6:18
16 Mawu Ofanana  

Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake.


Ahabu atamva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake, navala ziguduli ndi kusala chakudya. Anagona pa ziguduli, nayenda pangʼonopangʼono.


Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere.


Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze; amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.


Kumeneko, pa mitengo ya misondozi tinapachika apangwe athu,


Munagwira zikope zanga kuti ndisagone ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.


Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu.


Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje ndi kundiponya miyala;


Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.


Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona.


Mʼbandakucha, mfumu inanyamuka ndi kufulumira kupita ku dzenje la mikango lija.


Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba, oyimba zitoliro, ndi lipenga. Mwa iwe simudzapezekanso mʼmisiri wina aliyense. Mwa iwe simudzapezekanso phokoso la mphero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa