Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 6:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?” Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikize choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikiza choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 6:12
7 Mawu Ofanana  

“Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye.


Ndipo anthuwo anapita pamodzi kwa mfumu ndipo anati kwa iye, “Kumbukirani, inu mfumu kuti monga mwa lamulo la Amedi ndi Aperezi, palibe chimene mfumu inalamulira kapena kukhazikitsa chimasinthidwa.”


Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo limeneli ndipo musindikizepo dzina lanu kuti lisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sasinthidwa.”


Pamene ambuye a mtsikana uja anazindikira kuti chiyembekezo chawo chopezera ndalama chatha, anagwira Paulo ndi Sila nawakokera ku bwalo la akulu.


Chifukwa cha mawu amenewa woyangʼanira ndende anakawayika mʼchipinda chamʼkati mwa ndende, nawamangirira miyendo yawo mʼzigologolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa