Danieli 5:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Tsopano ndamva kuti iwe ukhoza kupereka matanthauzo ndi kuthetsa mavuto. Ngati ungawerenge zolembedwazi ndi kundiwuza tanthauzo lake, udzavekedwa chovala cha pepo ndi kuyikidwa mkanda wa golide mʼkhosi mwako, ndipo udzakhala wolamulira wachitatu mu ufumu uno.” Onani mutuwoBuku Lopatulika16 Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwo. Onani mutuwo |
Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”