Danieli 4:32 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Udzachotsedwa pakati pa anthu ndipo udzakhala ndi zirombo zakuthengo; udzadya udzu monga ngʼombe. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka iwe utavomereza kuti Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene iye afuna.” Onani mutuwoBuku Lopatulika32 Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; nizidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. Onani mutuwo |
Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna.