Danieli 4:17 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 “ ‘Angelo oyera ndiwo akutsimikiza chilangochi. Tsono anthu adziwe kuti Mulungu Wammwambamwamba ali ndi mphamvu yolamulira maufumu onse, ndipo amawapereka kwa aliyense akumufuna, ngakhale munthu wamba kuti alamulire.’ Onani mutuwoBuku Lopatulika17 Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu. Onani mutuwo |
Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna.