Danieli 4:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Anayankhula mofuwula kuti, ‘Gwetsa mtengo ndi kusadza nthambi zake; yoyola masamba ake kuti nyama zakuthengo zithawe pa mthunzi pake ndi mbalame zithawe pa nthambi zake. Onani mutuwoBuku Lopatulika14 Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama zakuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama za kuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake. Onani mutuwo |
“Inu mfumu munaona mthenga woyera, akuchokera kumwamba ndipo anati, ‘Gwetsani mtengo ndipo muwuwononge, koma musiye tsinde ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi unyolo wa chitsulo ndi mkuwa ndipo mulisiye pakati pa udzu wa mʼmunda. Mulole kuti linyowe ndi mame akumwamba. Likhale ngati nyama zakuthengo, mpaka zaka zidutse zisanu ndi ziwiri.’
Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna.