Danieli 3:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Aliyense amene sadzalambira ndi kupembedza adzaponyedwa nthawi yomweyo mʼngʼanjo ya moto.” Onani mutuwoBuku Lopatulika6 ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. Onani mutuwo |
Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”