Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 2:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika; amadziwa zimene zili mu mdima, ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

22 Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 2:22
37 Mawu Ofanana  

Yosefe anamuyankha Farao kuti, “Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna.”


Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.


Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu; chiwonongeko ndi chosaphimbidwa.


Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti


Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo.


Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo; mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.


Ndani angafanane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziwe kutanthauzira zinthu? Nzeru imabweretsa chimwemwe pa nkhope ya munthu ndipo imasintha maonekedwe ake awukali.


Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze zomwe zidzachitike mʼtsogolo. Tifotokozereni zinthu zamakedzana tiziganizire ndi kudziwa zotsatira zake. Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,


Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe, kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’ Palibe amene ananena, palibe analengeza zimenezi, palibe anamva mawu anu.


Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi, ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano; zinthuzo zisanaonekere Ine ndakudziwitsani.”


Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.


Kodi wina angathe kubisala Ine osamuona?” “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?” Akutero Yehova.


‘Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.’


Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.”


Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba,


Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”


Pali munthu wina mu ufumu wanu uno amene mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera. Pa nthawi ya ulamuliro wa abambo anu iye anapezeka kuti ali ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zonga za milungu. Mfumu Nebukadinezara, abambo anu, Ine ndikukuwuzani anamusankha iye kukhala mkulu wa amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula.


Ndamva kuti mzimu wa milungu uli mwa iwe ndi kuti uli ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zapadera.


Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo: “Ngakhale akupenya koma saona, ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira.


Kuwunika koona kumene kuwunikira munthu aliyense kunabwera ku dziko lapansi.


Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?” Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga.


Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”


Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.


chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri.


Ndi mkwiyo komanso ukali wake woopsa Yehova anawazula mʼdziko lawo ndi kuwaponyera mʼdziko lina, monga mmene zilili lero lino.”


Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.


Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.


Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.


Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa