Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 12:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma iweyo, Danieli, sungitsa mawuwa, umate bukuli kufikira nthawi ya chimaliziro. Anthu ambiri adzapita uku ndi uko ndipo nzeru zidzanka zikukulirakulira.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 12:4
25 Mawu Ofanana  

Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga pa phiri lopatulika la Yehova, pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.


Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”


Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.


Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.


Manga umboniwu ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.


“Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu, mudzionere nokha, funafunani mʼmabwalo ake. Ngati mungapeze munthu mmodzi amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi, ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.


Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.


Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”


Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”


“Amene ndi anzeru adzalangiza ambiri. Koma patapita kanthawi adzaphedwa ndi lupanga kapena kutenthedwa, kapena kugwidwa kapena kulandidwa katundu.


“Pa nthawi yomaliza mfumu yakummwera idzachita nkhondo ndi mfumu yakumpoto. Koma mfumu yakumpotoyi idzayikantha ndi magaleta ndi akavalo ndi sitima zapamadzi zambiri ngati mphepo yamkokomo. Idzalowa mʼmayiko ambiri ndikuwakokolola onse ngati madzi osefukira.


“Koma iweyo Danieli, pitiriza ndipo ulimbikire mpaka matsiriziro. Kenaka udzamwalira. Koma mʼmasiku otsiriza udzauka kuti ulandire gawo lako.”


Kenaka ine Danieli poyangʼana ndinaona anthu ena awiri atayima, wina tsidya lino la mtsinje, wina tsidya linalo.


Ndipo anandiyankha kuti, “Pita iwe Danieli, pakuti mawuwa ndi osungidwa ndi omatidwa kufikira nthawi ya chimaliziro.


Atayandikira kumene ndinayima, ndinachita mantha ndi kugwa chafufumimba. Iye anati, “Mwana wa munthu, zindikira kuti masomphenyawa akunena za nthawi yachimaliziro.”


Iye anati, “Ine ndikuwuza zimene zidzachitike ukadzatha mkwiyo, chifukwa masomphenyawa ndi a nthawi ya chimaliziro.”


“Masomphenya okhudza madzulo ndi mmawa amene unawaona aja ndi woona, koma uwasunge masomphenyawa mwachinsinsi popeza ndi onena za masiku a mʼtsogolo kwambiri.”


Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”


Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”


Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.”


Kenaka anandiwuza kuti, “Usabise mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili chifukwa nthawi yayandikira.


Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa