Danieli 12:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 “Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa. Onani mutuwoBuku Lopatulika1 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku. Onani mutuwo |
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.