Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 11:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iye adzalandanso milungu yawo, mafano awo achitsulo, ndi ziwiya zawo zamtengowapatali zasiliva ndi golide ndi kubwerera nazo ku Igupto. Adzaleka osayithira nkhondo mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasiliva ndi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasiliva ndi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:8
17 Mawu Ofanana  

Ndikudziwa kuti unachoka chifukwa unapukwa kufuna kubwerera kwanu kwa abambo ako. Koma nʼchifukwa chiyani unaba milungu yanga?”


Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga.


“Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova.


tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi ndiponso la mabwato onse okongola.


Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu.


Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira.


Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.


Kenaka mfumu ya kumpoto idzathira nkhondo dziko la mfumu ya kummwera koma idzalephera ndi kubwerera kwawo.


ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake, mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera, ikuwomba kuchokera ku chipululu. Kasupe wake adzaphwa ndipo chitsime chake chidzawuma. Chuma chake chonse chamtengowapatali chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.


Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya.


pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.


Mugumule maguwa awo ansembe, ndi kuphwanya miyala yawo yachipembedzo ndipo mutenthe pa moto mafano awo a Asera: mugwetse mafano a milungu yawo ndi kufafaniza mayina awo mʼmalo amenewo.


Iye anayankha kuti, “Inu mwanditengera milungu imene ndinapanga pamodzi ndi wansembe nʼkumapita. Tsono ine ndatsala ndi chiyani? Ndiye inu mungafunse kuti chavuta nʼchiyani?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa