Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 11:44 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Koma uthenga wochokera kummawa ndi kumpoto udzayiopsa, ndipo idzapita ndi ukali kukawononga ndi kutheratu anthu ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

44 Koma mbiri yochokera kum'mawa ndi kumpoto idzamvuta; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuononga konse ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Koma mbiri yochokera kum'mawa ndi kumpoto idzamvuta; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuononga konse ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:44
8 Mawu Ofanana  

“Kenaka mfumu yakummwera idzatuluka mokwiya ndi kumenya nkhondo ndi mfumu yakumpoto, imene idzasonkhanitsa gulu lalikulu la nkhondo, koma idzayigonjetsa.


Sitima zapamadzi zochokera ku mayiko a ku madzulo zidzalimbana naye, ndipo adzataya mtima. Kenaka idzabwerera mopsa mtima ndi kudzalimbana ndi chipembedzo cha anthu opatulika. Idzabwerera ndi kuchitira chifundo amene sadzasunga pangano loyera.


Idzalanda chuma cha golide, siliva, ndi zonse za mtengowapatali za ku Igupto, ndiponso anthu a ku Libiya ndi Akusi adzagonja kwa iwo.


Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”


Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa.


Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa